Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 9

Mfumu yaikazi ya ku Sheba acheza ndi Solomoni

1 Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa kuYerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndingamirazosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m’mtima mwake.

2 Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire.

3 Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga,

4 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.

5 Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m’dziko langa, ya machitidwe anu, ndi ya nzeru zanu.

6 Koma sindinakhulupirire mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva.

7 Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima chiimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu.

8 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.

9 Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.

10 Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomoni otenga golide ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali.

11 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneke zotere ndi kale lonse m’dziko la Yuda.

12 Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake.

Chuma ndi ulemerero wa Solomoni

13 Kulemera kwake tsono kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide;

14 osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndisilivakwa Solomoni.

15 Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri.

16 Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m’nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

17 Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona.

18 Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m’mbali mwa manjawo.

19 Ndi mikango khumi ndi iwiri inaimirirapo, mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwe wotere mu ufumu uliwonse.

20 Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zipangizo zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali za golide woona; siliva sanayesedwe kanthu m’masiku a Solomoni.

21 Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.

22 Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.

23 Ndipo mafumu onse a padziko lapansi anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake Mulungu adazilonga m’mtima mwake.

24 Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndimure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.

25 Ndipo Solomoni anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magaleta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m’mizinda ya magaleta, ndi mu Yerusalemu kwa mfumu.

26 Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito.

27 Ndipo mfumu inachulukitsa siliva mu Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu ili kumadambo kuchuluka kwake.

28 Ndipo anakamtengera Solomoni akavalo ku Ejipito, ndi ku maiko onse.

Kumwalira kwa Solomoni

29 Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwe kodi m’buku la mau a Natanimnenerindi m’zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m’masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati?

30 Ndipo Solomoni anakhala mfumu ya Israele yense mu Yerusalemu zaka makumi anai.

31 Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/9-190dc855d9078110cc5e389d48e0a5f8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *