Chonena Solomoni ndi pemphero lake popereka Kachisi
1 Pamenepo Solomoni anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani.
2 Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.
3 Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira.
4 Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m’kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti,
5 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m’dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse m’mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele;
6 Koma ndinasankhaYerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele.
7 Ndipo Davide atate wanga anafuna mumtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.
8 Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti unatero mumtima mwako;
9 koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzatuluka m’chuuno mwako, iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi.
10 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m’malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi.
11 Ndipo ndalongamo likasa, mulichipanganocha Yehova, anachichita ndi ana a Israele.
12 Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake.
13 Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m’litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;
14 nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu ngati Inu, m’mwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;
15 inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga chija mudamlonjezachi: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwachita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino.
16 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m’chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.
17 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.
18 Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu padziko lapansi? Taonani, thambo, inde m’mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga?
19 Chinkana chitero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kufuula ndi kupempha kwake, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu;
20 kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno.
21 Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israele, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire.
22 Munthu akachimwira mnansi wake, ndipo akamuikira lumbiro lakumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira ku guwa lanu la nsembe, m’nyumba ino;
23 pamenepo mumvere mu Mwamba, nimuchite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa chilungamo chake.
24 Ndipo anthu anu Israele akawakantha mdani chifukwa cha kukuchimwirani, nakabwerera iwowa ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m’nyumba ino;
25 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba, nimukhululukire tchimo la anthu anu Israele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
26 Mukatsekeka m’mwamba, mopanda mvula, chifukwa cha kukuchimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa;
27 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba, nimukhululukire tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israele, mutawalangiza njira yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale cholowa chao.
28 Mukakhala njala m’dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m’dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;
29 pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisraele, akadziwa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake, nakatambasulira manja ake kuloza kunyumba iyi:
30 pamenepo mumvere mu Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;
31 kuti aope Inu kuyenda m’njira zanu masiku onse akukhala iwo m’dziko limene munapatsa makolo athu.
32 Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israele, akafumira ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono ndi kupemphera kuloza kunyumba iyi;
33 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisraele; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu.
34 Akatulukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iliyonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza kumzinda uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu;
35 pamenepo mumvere mu Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.
36 Akachimwira Inu (pakuti palibe munthu wosachimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kunka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi;
37 koma akalingirira m’mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m’dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa;
38 akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m’dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mzinda mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi;
39 pamenepo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao; nimukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani.
40 Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.
41 Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino.
42 Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukire zachifundo za Davide mtumiki wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/6-ddac81d11a49dcff38e9643616b50664.mp3?version_id=1068—