Ahazi mfumu yoipitsitsa ya Yuda
1 Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake,
2 koma anayenda m’njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaalamafano oyenga.
3 Nafukizanso yekha m’chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m’moto, monga mwa zonyansa zaamitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.
4 Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira.
5 Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m’dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m’dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe aakulu.
6 Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao.
7 Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang’anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu.
8 Ndipo ana a Israele anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana aamuna ndi aakazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya.
9 Koma panalimneneriwa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m’dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.
10 Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu?
11 Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.
12 Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo,
13 nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele.
14 Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga msonkhano wonse.
15 Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mzinda wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.
16 Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize.
17 Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.
18 Afilisti omwe adagwa m’mizinda ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi midzi yake, ndi Timna ndi midzi yake, ndi Gimizo ndi midzi yake; nakhala iwo komweko.
19 Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.
20 Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.
21 Pakuti Ahazi analandako za m’nyumba ya Yehova ndi za m’nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo.
22 Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.
23 Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse.
24 Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m’nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m’nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m’ngodya zilizonse za Yerusalemu.
25 Ndi mu mzinda uliwonse wa Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake.
26 Machitidwe ena tsono, ndi njira zake zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.
27 Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m’mzinda wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/28-191073d70246bd322224cec858e35be3.mp3?version_id=1068—