Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 27

Yotamu mfumu ya Yuda

1 Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.

2 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe mu Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda.

3 Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu.

4 Namanga mizinda m’mapiri a Yuda, ndi m’nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe.

5 Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente asilivazana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe.

6 Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake.

7 Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m’buku la mafumu a Israele ndi Yuda.

8 Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi.

9 Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ake, namuika m’mzinda wa Davide; ndi Ahazi mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *