Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 25

Amaziya agonjetsa Aedomu

1 Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.

2 Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro.

3 Kunachitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ake amene adapha mfumu atate wake.

4 Koma sanaphe ana ao, koma anachita monga umo mulembedwa m’chilamulo, m’buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere tchimo lakelake.

5 Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa.

6 Analemberanso ngwazi zamphamvu za mu Israele zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente asilivazana limodzi.

7 Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu.

8 Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.

9 Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.

10 Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kuchokera ku Efuremu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.

11 Nalimbika mtima Amaziya. Natsogolera anthu ake, namuka ku Chigwa cha Mchere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.

12 Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.

13 Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera mizinda ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betehoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.

Amaziya alangidwa popembedza mafano

14 Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira.

15 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumiramneneriamene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditse anthu ao m’dzanja lanu?

16 Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.

17 Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani, tionane maso.

18 Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi.

19 Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.

20 Koma wosamvera Amaziya, pakuti ncha Mulungu ichi kuti awapereke m’dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.

21 Motero anakwera Yowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.

22 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawa yense kuhema kwake.

23 Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira Chipata cha Efuremu kufikira Chipata cha Kungodya, mikono mazana anai.

24 Natenga golide ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m’nyumba ya Mulungu kwa Obededomu, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwerera kunka ku Samariya.

25 Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.

26 Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwe kodi m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele?

27 Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu mu Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko.

28 Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ake m’mzinda wa Yuda.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/25-4ae1933dd7914293544961a4e41872b0.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *