Yehosafati apempha Yehova pa Amowabu ndi Aamoni
1 Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.
2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.
3 Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.
4 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumizinda yonse ya Yuda kufuna Yehova.
5 Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a kuYerusalemu, kunyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;
6 nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa mu Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse aamitundukodi? Ndi m’dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.
7 Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m’dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?
8 Nakhala m’mwemo iwowa, nakumangirani m’mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,
9 Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m’nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m’kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.
10 Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalole Israele awalowere, pakutuluka iwo m’dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;
11 tapenyani, m’mene atibwezera, kudzatiinga m’cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
12 Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
13 Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.
14 Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahaziele mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano;
15 nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
16 Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera chigwa chakuno cha chipululu cha Yeruwele.
17 Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.
18 Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala mu Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.
19 Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israele ndi mau omveketsa.
Amowabu ndi Aamoni akanthidwa
20 Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.
21 Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.
22 Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m’phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
23 Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m’phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala mu Seiri, anasandulikirana kuonongana.
24 Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.
25 Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.
26 Ndi tsiku lachinai anasonkhana m’chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino.
27 Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kunka ku Yerusalemu ndi chimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.
28 Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.
29 Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m’maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israele.
30 Nuchita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wake anampumulitsira pozungulirapo.
31 Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la make ndiye Azuba mwana wa Sili.
32 Ndipo anayenda m’njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.
33 Komatu misanje siinachotsedwe; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.
34 Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m’buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m’buku la mafumu a Israele.
35 Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa;
36 naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisisi, nazipanga zombozo mu Eziyoni-Gebere.
37 Pamenepo Eliyezere mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula ntchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisisi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/20-17ccf1fae3bb491409f9a51e8fe3e07c.mp3?version_id=1068—