Pangano pakati pa Yehosafati ndi Ahabu; afunsira kwa aneneri
1 Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu.
2 Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng’ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.
3 Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.
4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.
5 Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri aamuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m’dzanja la mfumu.
6 Koma Yehosafati anati, Kulibenso kunomneneriwa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?
7 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.
8 Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila.
9 Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.
10 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adzatha psiti.
11 Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m’dzanja la mfumu.
Mikaya anenera motsutsana nao
12 Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m’kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.
13 Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi.
14 Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Giliyadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzachita mwai; ndipo adzaperekedwa m’dzanja lanu.
15 Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane choonadi chokhachokha m’dzina la Yehova?
16 Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense kunyumba yake mumtendere.
17 Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzeni kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa?
18 Nati iye, Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lilikuima padzanja lake lamanja, ndi padzanja lake lamanzere.
19 Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israele ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Giliyadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.
20 Ndipo unatuluka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi chiyani?
21 Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m’kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene.
22 Ndipo tsono taonani, Yehova analonga mzimu wabodza m’kamwa mwa aneneri anu awa, nakunenetserani choipa Yehova.
23 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe?
24 Nati Mikaya, Tapenya, udzaona tsiku lolowa iwe m’chipinda cham’kati kubisala.
25 Ndipo mfumu ya Israele inati, Mumtenge Mikaya, mukambweze kwa Amoni kazembe wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu;
26 nimuziti, Itero mfumu, Mumuike uyu m’kaidi, ndi kumdyetsa chakudya chomsautsa, ndi kumwetsa madzi omsautsa, mpaka ndikabwera mumtendere.
27 Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananene mwa ine. Nati iye, Tamverani, anthu inu nonsenu.
Nkhondo iwakanika naphedwa Ahabu
28 Momwemo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera kunka ku Ramoti Giliyadi.
29 Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo.
30 Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magaleta ake, ndi kuti, Musayambana ndi ang’ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yekha.
31 Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke.
32 Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona kuti sanali mfumu ya Israele anabwerera osamtsatanso.
33 Ndipo munthu anaponya muvi wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israeleyo pakati pa maluma a malaya ake achitsulo. Potero anati kwa woyendetsa galetayo, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kukhamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.
34 Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israele inagwirizizika m’galeta wake popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/18-c3842ca5326a85b5ec4007925e6d2611.mp3?version_id=1068—