Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 14

Asa akantha Akusi

1 Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m’mzinda wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake; m’masiku ake dziko linaona bata zaka khumi.

2 Ndipo Asa anachita chokoma ndi choyenera m’maso mwa Yehova Mulungu wake,

3 nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,

4 nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kuchita chilamulo ndi chowauza Iye.

5 Anachotsanso m’mizinda yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake.

6 Ndipo anamanga mizinda yamalinga mu Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.

7 Ndipo anati kwa Yuda, Timange mizinda iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.

8 Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a mu Yuda zikwi mazana atatu; ndi a mu Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.

9 Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.

10 Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m’chigwa cha Zefati ku Maresa.

11 Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m’dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.

12 Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.

13 Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.

14 Ndipo anakantha mizinda yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m’mizinda monse, pakuti mudachuluka zofunkha m’menemo.

15 Anakanthanso a m’mahema a ng’ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndingamira; nabwerera kunka kuYerusalemu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/14-60d7db5b8d612448ac8e7007a9492ae2.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *