Sisake wa ku Ejipito athira nkhondo Rehobowamu
1 Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye.
2 Ndipo Rehobowamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisake mfumu ya ku Ejipito anakwereraYerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova.
3 Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka mu Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi.
4 Ndipo analanda mizinda yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu.
5 Pamenepo Semayamnenerianadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m’dzanja la Sisake.
6 Pamenepo akalonga a Israele ndi mfumu anadzichepetsa, nati, Yehova ali wolungama.
7 Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake.
8 Koma adzakhala akapolo ake, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.
Sisake alanda chuma cha Kachisi ndi cha nyumba ya mfumu
9 Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m’nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.
10 Ndipo Rehobowamu mfumu anapanga m’malo mwa izi zikopa zamkuwa, nazipereka m’manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.
11 Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m’nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku chipinda cha olindirira.
12 Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma mu Yuda.
13 Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu mu Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, ndiwo mzinda Yehova adausankha m’mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.
14 Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova.
15 Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.
16 Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa m’mzinda wa Davide; ndipo Abiya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/12-922e6211e9852a9882ef392494f0b7a4.mp3?version_id=1068—