Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 7

1 Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya.

2 Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m’mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.

Akhate anai awulula za kuthawa Aaramu

3 Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?

4 Tikati, Tilowe m’mzinda, m’mzinda muli njala, tidzafa m’mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.

5 Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.

6 Popeza Ambuye adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere.

7 Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao.

8 Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m’hema mmodzi, nadya namwa, natengakosilivandi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m’hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.

9 Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m’nyumba ya mfumu.

10 Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.

11 Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m’nyumba ya mfumu.

12 Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m’mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m’misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m’mzinda tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m’mzindamo.

13 Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m’mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione.

14 Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone.

15 Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m’njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m’kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.

16 Natuluka anthu, nafunkha m’misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova.

17 Koma mfumu idayang’anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira padzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu.

18 Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya;

19 ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angachite mazenera m’mwamba, chikachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ichi ndi maso ako, koma osadyako ai;

20 kudamchitikira momwemo; popeza anthu anampondereza pachipata nafa iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/7-8517cc8607b698666ebc4801cda98146.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *