Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 3

Chipulumutso chodabwitsa cha nkhondo za Yuda, Israele, ndi Edomu

1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m’chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

2 Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa chaBaalaadachipanga atate wake.

3 Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.

4 Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.

5 Koma kunachitika, atafa Ahabu mfumu ya Mowabu anapandukana ndi mfumu ya Israele.

6 Ndipo mfumu Yehoramu anatuluka mu Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisraele onse.

7 Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.

8 Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu.

9 Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

10 Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m’dzanja la Mowabu.

11 Koma Yehosafati anati, Palibe panomneneriwa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m’manja a Eliya.

12 Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo. Pamenepo mfumu ya Israele, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.

13 Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m’dzanja la Mowabu.

14 Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang’anitsani, kapena kukuonani.

15 Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, wanthetemyayo ali chiimbire, dzanja la Yehova linamgwera.

16 Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m’chigwa muno mukhale maenje okhaokha.

17 Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma chigwacho chidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng’ombe zanu, ndi zoweta zanu.

18 Ndipo ichi chidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amowabu m’dzanja lanu.

19 Ndipo mudzakantha mizinda yonse ya malinga, ndi mizinda yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.

20 Ndipo kunachitika m’mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.

21 Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m’chuuno ndi okulapo, naima iwo m’malire.

22 Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amowabu madzi ali pandunji pao ali psu ngati mwazi;

23 nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzake; ndipo tsopano, tiyeni Amowabu inu, tikafunkhe.

24 Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israele, Aisraele ananyamuka, nakantha Amowabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m’dziko ndi kukantha Amowabu.

25 Napasula mizinda, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake mu Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.

26 Ndipo ataona mfumu ya Mowabu kuti nkhondo idamuvuta, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoze.

27 Pamenepo anagwira mwana wake wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m’malo mwake, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israele kwambiri; potero anamchokera, nabwerera ku dziko lao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/3-122ee4c7781c1bb9cddfbe4fdf28cbdb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *