Yerusalemu apasulidwa, anthu natengedwa kunka ku Babiloni
1 Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzeraYerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.
2 Ndipo mzindawo unazingidwa ndi timalinga mpaka chaka chakhumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya.
3 Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m’mzindamo, panalibe chakudya kwa anthu a m’dzikomo.
4 Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.
5 Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, nayipeza m’zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.
6 Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula, naweruza mlandu wake.
7 Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.
8 Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu,
9 natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.
10 Ndi khamu lonse la Ababiloni linali ndi mkulu wa olindirira linagumula linga la Yerusalemu louzinga.
11 Ndi anthu otsalira m’mzinda, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.
12 Koma mkulu wa olindirira anasiya osaukadi a m’dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi.
13 Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m’nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m’nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni.
14 Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.
15 Ndi zopalira moto, ndi mbale zowazira za golide yekhayekha, ndi zasilivayekhayekha, mkulu wa asilikali anazichotsa.
16 Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomoni, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoze kuyesa kulemera kwake.
17 Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.
18 Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu;
19 natenga m’mzindamo mdindo woikidwa woyang’anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m’mzindamo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m’dziko; ndi anthu a m’dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m’mzindamo.
20 Ndipo Nebuzaradani mkulu wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula.
21 Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m’dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m’dziko lao.
Gedaliya wolamulira mu Yerusalemu aphedwa ndi Ismaele
22 Koma kunena za anthu otsalira m’dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.
23 Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.
24 Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Ababiloni; khalani m’dziko; tumikirani mfumu ya Babiloni, ndipo kudzakukomerani.
25 Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa.
26 Pamenepo ananyamuka anthu onse aang’ono ndi aakulu, ndi akazembe a makamu, nadza ku Ejipito; pakuti anaopa Ababiloni.
27 Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m’kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;
28 nakamba naye zokoma, namkweza mpando wake waulemu upose mipando ya mafumu anali pamodzi naye mu Babiloni.
29 Nasintha zovala zake za m’kaidi, namadya iye mkate pamaso pake masiku onse a moyo wake.
30 Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/25-f076b948b51a7a609962fda8c98bcb09.mp3?version_id=1068—