1 Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.
2 Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.
3 Zedi ichi chinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwachotsa pamaso pake, chifukwa cha zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazichita;
4 ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzazaYerusalemundi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.
5 Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
6 Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.
7 Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezenso kutuluka m’dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.
Ayamba kutengedwa ukapolo kunka ku Babiloni
8 Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
9 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita atate wake.
10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mzindawo misasa.
11 Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babiloni kumzinda, ataumangira misasa anyamata ake,
12 Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
13 Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.
14 Nachoka nao a mu Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m’dziko.
15 Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m’dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.
16 Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.
17 Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m’malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.
Zedekiya mfumu yotsiriza ya Yuda
18 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
19 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yehoyakimu.
20 Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika mu Yerusalemu ndi mu Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/24-bcd12fd621ef038c342d14527c9fc502.mp3?version_id=1068—