Manase woipitsitsa
1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba.
2 Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa zaamitunduamene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.
3 Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsiraBaalamaguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4 Namanga iye maguwa a nsembe m’nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, Mu Yerusalemu ndidzaika dzina langa.
5 Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m’mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.
6 Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.
7 Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m’nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M’nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.
8 Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m’dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga.
9 Koma sanamvere, nawalakwitsa Manase, nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israele.
10 Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ake aneneri, ndi kuti,
11 Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake;
12 chifukwa chake atero Yehova Mulungu wa Israele, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda choipa, chakuti yense achimvera chidzamliritsa mwini khutu.
13 Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira.
14 Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m’dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;
15 popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.
16 Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
17 Machitidwe ena tsono a Manase, ndi zochimwa zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
18 Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m’munda wa nyumba yake, m’munda wa Uza, nakhala mfumu m’malo mwake Amoni mwana wake.
Amoni mfumu ya Yuda
19 Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.
20 Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo amachitira Manase atate wake.
21 Nayenda iye m’njira monse anayendamo atate wake, natumikira mafano anawatumikira atate wake, nawagwadira;
22 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m’njira ya Yehova.
23 Ndipo anyamata ake a Amoni anamchitira chiwembu, napha mfumuyo m’nyumba yakeyake.
24 Koma anthu a m’dzikomo anapha onse akumchitira chiwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m’dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wake m’malo mwake.
25 Machitidwe ena tsono a Amoni adawachita, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
26 Naikidwa iye m’manda mwake m’munda wa Uza; nakhala mfumu m’malo mwake Yosiya mwana wake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/21-c236c48a7cb1dc7ca11b38ad0fd6a2f4.mp3?version_id=1068—