Nkhawa ya Hezekiya ndi pemphero lake
1 Ndipo kunali, atamva mfumu Hezekiya, anang’amba zovala zake, nafundira chiguduli, nalowa m’nyumba ya Yehova.
2 Natuma Eliyakimu woyang’anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesayamnenerimwana wa Amozi.
3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.
4 Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.
5 Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.
6 Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asiriya anandichitira nao mwano.
7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m’dziko lake.
8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.
9 Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,
10 Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti,Yerusalemusudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.
11 Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?
12 Kodi milungu yaamitunduinawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala mu Telasara?
13 Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?
14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.
15 Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati paakerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.
17 Zoona, Yehova, mafumu a Asiriya anapasula amitundu ndi maiko ao,
18 naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; chifukwa chake anaiononga.
19 Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m’dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.
Yesaya amtonthoza mtima Hezekiya
20 Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Chondipempha iwe pa Senakeribu mfumu ya Asiriya ndachimva.
21 Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi waZiyoniakunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.
22 Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m’mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.
23 Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m’ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.
24 Ndakapa, ndamwa madzi achilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Ejipito.
25 Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula mizinda yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.
26 Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wakuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.
27 Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.
28 Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m’makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m’mphuno mwako, ndi cham’kamwa changa m’milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.
29 Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.
30 Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.
31 Pakuti ku Yerusalemu kudzatuluka otsala, ndi akupulumukawo kuphiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi.
32 Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m’mzinda muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.
33 Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m’mzinda muno, ati Yehova.
34 Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.
Mthenga wa Yehova awapha Aasiriya
35 Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.
36 Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive.
37 Ndipo kunali popembedza iye m’nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/19-aea863c5c1572d087d92c2107d71efd2.mp3?version_id=1068—