Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 18

Hezekiya wabwino akhazikanso chipembedzo cha Yehova

1 Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai muYerusalemu; ndi dzina la make ndiye Abi mwana wa Zekariya.

3 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake.

4 Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

6 Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7 Ndipo Yehova anali naye, nachita iye mwanzeru kulikonse anamukako, napandukira mfumu ya Asiriya osamtumikira.

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mzinda walinga.

9 Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10 Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya.

11 Ndipo mfumu ya Asiriya anachotsa Aisraele kunka nao ku Asiriya, nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m’mizinda ya Amedi;

12 chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwirachipanganochake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.

Senakeribu amangira Yerusalemu misasa

13 Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera mizinda yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14 Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu asilivandi matalente makumi atatu a golide.

15 Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m’nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu.

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya.

17 Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku Malo a Wotsuka Thonje.

18 Ndipo m’mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19 Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Chikhulupiriro ichi nchotani uchikhulupirira?

20 Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?

21 Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzampyoza dzanja lake; ateroFaraomfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.

22 Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?

23 Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24 Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata aang’ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo?

25 Ngati ndakwerera malo ano wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu mu Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe mu Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.

27 Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28 Naima kazembeyo, nafuula ndi mau aakulu mu Chiyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikulu mfumu ya Asiriya.

29 Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m’dzanja lake;

30 kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mzinda uwu sudzaperekedwa m’dzanja la mfumu ya Asiriya.

31 Musamvere Hezekiya; pakuti itero mfumu ya Asiriya, Mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wake, ndi yense ku mkuyu wake, ndi kumwa yense madzi a m’chitsime chake;

32 mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko laazitonandi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.

33 Kodi mulungu uliwonse waamitunduwalanditsa dziko lake m’dzanja la mfumu ya Asiriya ndi kale lonse?

34 Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m’dzanja langa?

35 Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m’dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m’dzanja langa?

36 Koma anthuwo anakhala chete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

37 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang’anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong’ambika, namuuza mau a kazembeyo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/18-7287d1aa3800a05d802ca33cdb0cfbe8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *