Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 11

Ataliya apha achifumu onse, Yowasi apulumuka

1 Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.

2 Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m’chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.

3 Nakhala naye wobisika m’nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

4 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m’nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.

5 Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa paSabatalizilindira nyumba ya mfumu,

6 ndi lina lizikhala ku chipata cha Suri, ndi lina ku chipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuitchinjiriza.

7 Ndipo magawo awiri a inu, ndiwo onse otulukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.

8 Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m’manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye.

9 Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m’nyumba ya Yehova.

11 Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m’manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12 Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m’manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.

13 Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m’nyumba ya Yehova;

14 napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m’dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang’amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.

15 Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang’anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m’nyumba ya Yehova.

16 Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

Pangano la Yehoyada wansembe

17 Ndipo Yehoyada anachitachipanganopakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

18 Namuka anthu onse a m’dzikomo kunyumba yaBaala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang’anira nyumba ya Yehova.

19 Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m’dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu.

20 Nakondwerera anthu onse a m’dziko, ndi m’mzinda munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu.

21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/11-4ba17fef3ffb7bf5dbcc293ffc28e9b5.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *