Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 10

Yehu aononga mbumba ya Ahabu

1 Ndipo Ahabu anali nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri mu Samariya. Nalemba makalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

2 Tsono ikakufikani inu kalata iyi, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mizinda yalinga, ndi zida,

3 musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.

4 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji?

5 Ndipo iye wakuyang’anira nyumba, ndi iye wakuyang’anira mzinda, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani.

6 Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m’mzinda, amene anawalera.

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m’madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.

8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m’mawa.

9 Ndipo kunali m’mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu mu Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense.

12 Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira,

13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu.

14 Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense.

Aphedwa aneneri a Baala

15 Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M’mwemo anamuyendetsa m’galeta wake.

17 Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.

18 Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikiraBaalapang’ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19 Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20 Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m’nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.

22 Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala.

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m’nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

24 Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m’manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake.

25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumzinda wa nyumba ya Baala.

26 Natulutsa zoimiritsa zija zinali m’nyumba ya Baala, nazitentha.

27 Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

28 Momwemo Yehu anaononga Baala mu Israele.

Yehu apembedza mafano

29 Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang’ombe agolide okhala mu Betele ndi mu Dani.

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m’mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.

31 Koma Yehu sanasamalire kuyenda m’chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele.

32 Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m’malire onse a Israele,

33 kuyambira ku Yordani kum’mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani.

34 Ndipo machitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazichita, ndi mphambu yake yonse, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

35 Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika mu Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

36 Ndipo masiku ake akukhala Yehu mfumu ya Israele mu Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/10-d1e186fb1aa681d106f89ab885c7e630.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *