1 Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;
2 pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kutiAkayaanakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.
3 Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m’menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu;
4 kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m’kulimbika kumene.
5 Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.
6 Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta.
7 Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.
8 Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
9 monga kwalembedwa,
Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka;
chilungamo chake chikhale kunthawi yonse.
10 Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu;
11 polemeretsedwa inu m’zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
12 Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;
13 popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino waKhristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
14 ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu.
15 Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/9-5838a978a1e6dc31be2fcc956b07afcf.mp3?version_id=1068—