Categories
2 AKORINTO

2 AKORINTO 8

Chipereko cha kwa Akhristu aumphawi a ku Yerusalemu

1 Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwaMipingoya ku Masedoniya,

2 kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

3 Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yao,

4 anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;

5 ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.

6 Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.

7 Koma monga muchulukira m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mau, ndi m’chidziwitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m’chisomo ichi.

8 Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso.

9 Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu YesuKhristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

10 Ndipo m’menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.

11 Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m’chimene muli nacho.

12 Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.

13 Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe;

14 koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu.

15 Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalire; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichinamsowe.

16 Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

17 Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake.

18 Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli mu Mipingo yonse;

19 ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m’chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;

20 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;

21 pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

22 Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m’zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu.

23 Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.

24 Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/8-6d21823f6abb21f2ae46439c7efd2c04.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *