1 Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.
2 Pakutinso m’menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba;
3 ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche.
4 Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.
5 Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu.
6 Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m’thupi, sitili kwa Ambuye.
7 (Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe);
8 koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m’thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.
9 Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye.
10 Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza waKhristu, kuti yense alandire zochitika m’thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Utumiki wa chiyanjanitso
11 Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m’zikumbu mtima zanu.
12 Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
13 Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.
14 Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa;
15 ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka.
16 Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
17 Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
18 Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso;
19 ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
20 Chifukwa chake tili atumiki m’malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m’malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
21 Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m’malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/5-62a841973f31974eb932ff57b097646f.mp3?version_id=1068—