1 Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?
2 Inu ndinu kalata yathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;
3 popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata yaKhristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m’magome amiyala, koma m’magome a mitima yathupi.
4 Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu:
5 si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;
6 amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo.
7 Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m’miyala, unakhala mu ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang’anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:
8 koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala mu ulemerero?
9 Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.
10 Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwe cha ulemerero m’menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo.
11 Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili mu ulemerero.
12 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,
13 ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang’anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;
14 koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.
15 Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao.
16 Koma pamene akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chichotsedwa.
17 Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu.
18 Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CO/3-6a88c6d8f884f0eb8f463b4c541c9820.mp3?version_id=1068—