Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO Mau Oyamba

Mau Oyamba

Timoteo anali Mkhristu wachinyamata wa ku Asiya, mai wake anali Myuda koma bambo wake anali Mgriki. Paulo adamtenga kuti amperekeze pa maulendo ake ndi kumthandiza pa ntchito yolalika. Pomulembera kalatayi, Paulo afuna kumchenjeza pa zophunzitsa zina zabodza zimene zikusokoneza mpingo. Anthu ena ophatikiza nzeru zina zachiyuda ndi zina zachikunja ankati dziko lapansi monga lilirimu nloipa, ndipo palibe munthu angapulumuke akapanda kuphunzira nzeru zina zobisika ndi kutsata miyambo ina, monga kusala zakudya zina ndi zina ndi kuletsa maukwati. Paulo akuperekanso malangizo pa chipembedzo, za kayendetsedwe ka mpingo ndi za makhalidwe ofunika kwa atsogoleri. Akumuuzanso kuti iye ayesetse kukhala mtumiki wokhulupirika pa udindo wake woyang’anira magulu onse a Akhristu.

Za mkatimu

Mau oyamba 1.1-2

Malangizo okhudza mpingo ndi atsogoleri ake 1.3—3.16

Malangizo kwa Timoteo pa ntchito yake 4.1—6.21

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *