Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 6

Zoyenera akapolo

1 Onse amene ali akapolo a m’goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.

2 Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze.

Zochenjeza zina

3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu YesuKhristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:

4 iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;

5 makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.

6 Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu;

7 pakuti sitinatenge kanthu polowa m’dziko lapansi, ndiponso sitingathe kupita nako kanthu pochoka pano;

8 koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimene zitikwanire.

9 Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chionongeko ndi chitayiko.

10 Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

11 Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.

12 Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri.

13 Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;

14 kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu;

15 limene adzalionetsa m’nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;

16 amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m’kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha.Amen.

17 Lamulira iwo achuma m’nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;

18 kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

19 nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.

20 Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama;

21 chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/6-a789bb02dcbaf3472b214cc55a04588e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *