Chipanduko cha m’masiku otsiriza
1 Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m’masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda,
2 m’maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m’chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;
3 a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.
4 Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;
5 pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.
A utumiki akhale okhulupirika ndi achangu
6 Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino waKhristuYesu, woleredwa m’mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;
7 koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo;
8 pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.
9 Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.
10 Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.
11 Lamulira izi, nuziphunzitse.
12 Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m’mau, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.
13 Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza.
14 Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.
15 Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.
16 Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/4-3ed6b410f224e7cba00a2613b8e541d9.mp3?version_id=1068—