Zoyenera oyang’anira ndi atumiki
1 Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.
2 Ndipo kuyenera woyang’anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
3 wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;
4 woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse.
5 Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanjiMpingowa Mulungu?
6 Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.
7 Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.
8 Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa;
9 okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m’chikumbu mtima choona.
10 Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa.
11 Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m’zonse.
12 Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m’nyumba yao ya iwo okha.
13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m’chikhulupiriro cha mwaKhristuYesu.
14 Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa,
15 kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m’nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.
16 Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m’thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndiangelo, analalikidwa mwaamitundu, wokhulupiridwa m’dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/3-c6233ce223962c42de2485e6178a692f.mp3?version_id=1068—