Categories
1 TIMOTEO

1 TIMOTEO 2

Pemphero la kwa anthu onse

1 Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;

2 chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m’moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi m’kulemekezeka monse.

3 Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;

4 amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.

5 Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu,KhristuYesu,

6 amene anadzipereka yekha chiombolo m’malo mwa onse; umboni m’nyengo zake;

7 umene anandiika ine mlaliki wake ndimtumwi(ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi waamitundum’chikhulupiriro ndi choonadi.

8 Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.

Zoyenera akazi

9 Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

10 komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.

11 Mkazi aphunzire akhale wachete m’kumvera konse.

12 Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.

13 PakutiAdamuanayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14 ndipo Adamu sananyengedwe, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m’kulakwa;

15 koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m’chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1TI/2-0a8170af0d1cfbfedbd854c5012a08a6.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *