Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 6

Afilisti abweza likasa ku dziko la Aisraele

1 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.

2 Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.

3 Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka.

4 Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.

5 Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.

6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndiFaraoanaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?

7 Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng’ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng’ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;

8 ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m’bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.

9 Ndipo muyang’anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.

10 Ndipo anthuwo anatero; natenga ng’ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao;

11 naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m’mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.

12 Ndipo ng’ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.

13 Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m’chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona.

14 Ndipo galetalo linafika m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng’ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.

15 Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m’mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.

16 Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo.

17 Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;

18 ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m’munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.

19 Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m’likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.

Likasa lisungidwa ku Kiriyati-Yearimu

20 Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?

21 Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/6-9ca9e6ba1aaac566a6452163c956e7f0.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *