Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 3

Masomphenya a Samuele

1 Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke.

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m’malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m’mene munali likasa la Mulungu.

4 Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano.

5 Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitane, kagone. Napita iye, nagona.

6 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitane, mwana wanga; kagone.

7 Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye.

8 Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo.

9 Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m’malo mwake.

10 Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva.

11 Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.

12 Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.

13 Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.

14 Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse.

Samuele awulula kwa Eli

15 Ndipo Samuele anagona kufikira m’mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.

16 Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine.

17 Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe.

18 Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.

19 Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe.

20 Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhalemneneriwa Yehova.

21 Ndipo Yehova anaonekanso mu Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/3-14d33f035d75dac34878bfdce1045d58.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *