Davide alekanso Saulo osamupha
1 Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m’phiri la Hakila, kupenya kuchipululu!
2 Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m’chipululu cha Zifi.
3 Saulo namanga zithando m’phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko.
4 Chifukwa chake Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Saulo anabwera ndithu.
5 Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.
6 Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.
7 Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m’kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye.
8 Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m’dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.
9 Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?
10 Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.
11 Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.
12 Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m’tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse.
13 Ndipo Davide anaolokera kutsidya, naima patali pamwamba paphiri; pakati pao panali danga lalikulu;
14 ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?
15 Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.
16 Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikire mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti?
17 Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga.
18 Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m’dzanja langa muli choipa chotani?
19 Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.
20 Chifukwa chake tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutali ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israele yatuluka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri.
21 Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.
22 Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga.
23 Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m’dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.
24 Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.
25 Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/26-b98ae642e4e59491a07ac35012ffd8a8.mp3?version_id=1068—