Zoyenera akulu ndi anyamata; adzichepetse, adikire
1 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa zaKhristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:
2 Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang’anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;
3 osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.
4 Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.
5 Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
6 Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
7 ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.
8 Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
9 ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.
10 Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
11 Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi.Amen.
12 Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m’chimenechi muimemo.
13 Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akukupatsani moni; ateronso Marko mwana wanga.
14 Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi.
Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/5-25fadd4395781cab59ea834bbbd162f1.mp3?version_id=1068—