1 PopezaKhristuadamva zowawa m’thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m’thupi walekana nalo tchimo;
2 kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m’thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.
3 Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro chaamitundu, poyendayenda inu m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
4 m’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano;
5 amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.
6 Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.
7 Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m’mapemphero;
8 koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
9 mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:
10 monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
11 akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m’zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi.Amen.
12 Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu:
13 koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.
14 Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.
15 Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;
16 koma akamva zowawa ngati Mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.
17 Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?
18 Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?
19 Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m’manja a Wolenga wokhulupirika.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/4-ed7d7b89bc35350a2703baa0e8242e8e.mp3?version_id=1068—