Categories
1 PETRO

1 PETRO 1

1 Petro,mtumwiwa YesuKhristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,

2 monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m’chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.

Chiyamiko chifukwa cha chipulumutso

3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;

4 kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira mu Mwamba inu,

5 amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.

6 M’menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu,

7 kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

8 amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:

9 ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu.

10 Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani;

11 ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.

12 Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu iziangeloalakalaka kusuzumiramo.

Awadandaulira atsate kuyera mtima

13 Mwa ichi, podzimanga m’chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m’vumbulutso la Yesu Khristu;

14 monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

15 komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m’makhalidwe anu onse;

16 popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

17 Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;

18 podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndisiliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu:

19 koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wamwanawankhosawopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:

20 amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi,

21 chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.

22 Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;

23 inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

24 Popeza,

Anthu onse akunga udzu,

ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu.

Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;

25 koma Mau a Ambuye akhala chikhalire.

Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1PE/1-43096c9571a0529f5c5a13314c96a8ee.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *