Categories
1 MBIRI

1 MBIRI Mau Oyamba

Mau Oyamba

Mabuku awiri otchedwa

Mbiri

akambanso zina ndi zina zimene zidakambidwa kale m’mabuku a

Samuele

ndi a

Mafumu

; koma kakambidwe kake nkosiyaniranapo polongosola mbiri ya ufumu wa Israele, chifukwa olemba mabuku a

Mbiri

ali ndi zolinga ziwiri:

1. Afuna kuwonetsa kuti, ngakhale Israele ndi a Yuda adawonongeka kotheratu, Mulungu salephera kuchita zimene analonjeza, mwakuti akuwongolerabe zinthu kudzera mwa anthu okhala mu Yuda, monga momwe adaziganiziratu pa chiyambi. Pofuna kulimbikitsa chiyembekezo chimenechi, olemba mabukuwa akukumbutsa zazikulu zimene adachita Davide ndi Solomoni, ndiponso ntchito za Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya, zothandiza anthu kukhala okhulupirika kwa Mulungu.

2. Afunanso kulongosola za chiyambi cha chipembedzo mu Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu, ndiponso za udindo wa ansembe ndi Alevi pa mwambo wa chipembedzo. M’mabuku awiriwo Davide akuwoneka kuti iye ndi mkulu woyambitsa zonsezi, ngakhale amene anamanga Kachisi wa Yehova anali Solomoni.

Buku loyamba la

Mbiri

lifotokoza makamaka za ufumu wa Davide.

Za mkatimu

Mndandanda wa anthu akale ndiponso wa makolo a Israele

1.1—9.44

Imfa ya Saulo

10.1-14

Ufumu wa Davide

11.1—29.30

a. Mavuto ake ndipo ntchito za zazikulu

11.1—22.1

b. Zokonzekera kumanga Kachisi wa Yehova

22.2—29.30

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *