Adzukulu a Isakara
1 Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Puwa, Yasubu ndi Simironi; anai.
2 Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m’mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.
3 Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaele, ndi Obadiya, ndi Yowele, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akulu.
4 Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi, popeza anachuluka akazi ao ndi ana ao.
5 Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa chibadwidwe chao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
Adzukulu a Benjamini ndi Nafutali
6 Ana a Benjamini ndiwo Bela, ndi Bekere, ndi Yediyaele, atatu.
7 Ndi ana a Bela: Eziboni, ndi Uzi, ndi Uziyele, ndi Yerimoti, ndi Iri, asanu; akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m’mabuku a chibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai.
8 Ndi ana a Bekere: Zimira, ndi Yowasi, ndi Eliyezere, ndi Eliyoenai, ndi Omuri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekere.
9 Ndipo anayesedwa mwa chibadwidwe chao, mwa mibadwo yao, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi makumi awiri mphambu mazana awiri.
10 Ndi mwana wa Yediyaele: Bilihani; ndi ana a Bilihani: Yeusi, ndi Benjamini, ndi Ehudi, ndi Kenana, ndi Zetani, ndi Tarisisi, ndi Ahisahara.
11 Onsewa ndiwo ana a Yediyaele; ndiwo akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akutuluka kugulu kunkhondo.
12 Supimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.
13 Ana a Nafutali: Yaziyele, ndi Guni, ndi Yezere, ndi Salumu, ana a Biliha.
Adzukulu a Manase
14 Ana a Manase ndiwo Asiriele amene mkazi wake anambala. Koma mkazi wake wamng’ono Mwaramu anabala Makiri atate wa Giliyadi;
15 ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wake wa Hupimu ndi Supimu, dzina lake ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana wachiwiri wa Manase ndiye Zelofehadi. Ndi Zelofehadi anali ndi ana aakazi.
16 Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namutcha dzina lake Peresi, ndi dzina la mbale wake ndiye Seresi, ndi ana ake ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.
17 Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Giliyadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.
18 Ndi mlongo wake Hamoleketi anabala Isihodi, ndi Abiyezere, ndi Mala.
19 Ndi ana a Semida ndiwo Ahiyani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniyamu.
A Efuremu
20 Ndi ana a Efuremu: Sutela, ndi Beredi mwana wake, ndi Tahati mwana wake, ndi Eleada mwana wake, ndi Tahati mwana wake,
21 ndi Zabadi mwana wake, ndi Sutela mwana wake, ndi Ezere, ndi Eleadi, amene anthu a Gati obadwa m’dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.
22 Ndipo Efuremu atate wao, anachita maliro masiku ambiri, ndi abale ake anadza kudzamtonthoza mtima.
23 Ndipo analowa kwa mkazi wake, naima iye, nabala mwana, namutcha dzina lake Beriya, popeza m’nyumba mwake mudaipa.
24 Ndipo mwana wake wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Betehoroni wa kunsi, ndi Betehoroni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.
25 Ndipo Refa anali mwana wake, ndi Resefi, ndi Tela mwana wake, ndi Tahani mwana wake,
26 Ladani mwana wake, Amihudi mwana wake, Elisama mwana wake,
27 Nuni mwana wake, Yoswa mwana wake.
28 Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Betele ndi midzi yake, ndi kum’mawa Naarani, ndi kumadzulo Gezere ndi midzi yake, ndi Sekemu ndi midzi yake, mpaka Aya ndi midzi yake;
29 ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi midzi yake, Taanaki ndi midzi yake, Megido ndi midzi yake, Dori ndi midzi yake. M’menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
30 Ana a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao.
31 Ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele, ndiye atate wa Birizaiti.
32 Ndi Hebere anabala Yafileti, ndi Somere, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao.
33 Ndi ana a Yafileti: Pasaki, ndi Bimala, ndi Asivati. Awa ndi ana a Yafileti.
34 Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu.
35 Ndi ana a Helemu mbale wake: Zofa, ndi Imina, ndi Selesi, ndi Amala.
36 Ana a Zofa: Suwa, ndi Harenefere, ndi Suwala, ndi Beri, ndi Imira,
37 Bezere, ndi Hodi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.
38 Ndi ana a Yetere: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.
39 Ndi ana a Ula: Ara, ndi Haniyele, ndi Riziya.
40 Awa onse ndiwo ana a Asere, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akulu mwa akalonga. Oyesedwa mwa chibadwidwe chao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/7-41a092f5408252ab37e1d270a1c9bba8.mp3?version_id=1068—