Adzukulu a Rubeni
1 Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m’buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.
2 Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
3 ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele: Hanoki, ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi.
4 Ana a Yowele: Semaya mwana wake, Gogi mwana wake, Simei mwana wake,
5 Mika mwana wake, Reaya mwana wake, Baala mwana wake,
6 Beera mwana wake, amene Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.
7 Ndi abale ake monga mwa mabanja ao, powerenga chibadwidwe cha mibadwo yao: akulu ndiwo Yeiyele, ndi Zekariya,
8 ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni;
9 ndi kum’mawa anakhala mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Yufurate; pakuti zoweta zao zinachuluka m’dziko la Giliyadi.
10 Ndipo masiku a Saulo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m’mahema mwao kum’mawa konse kwa Giliyadi.
Adzukulu a Gadi
11 Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m’dziko la Basani mpaka Saleka:
12 Yowele mkulu wao, ndi Safamu wachiwiri, ndi Yanai, ndi Safati mu Basani;
13 ndi abale ao a nyumba za makolo ao: Mikaele, ndi Mesulamu, ndi Sheba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri.
14 Awa ndi ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikaele, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi,
15 Ahi mwana wa Abidiyele, mwana wa Guni, ndiye mkulu wa nyumba za makolo ao.
16 Ndipo anakhala mu Giliyadi mu Basani, ndi m’midzi yake, ndi podyetsa pake ponse pa Saroni, mpaka malire ao.
17 Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a chibadwidwe chao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m’masiku a Yerobowamu mfumu ya Israele.
18 Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira chikopa ndi lupanga, ndi kuponya mivi, ozolowera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akutuluka kunkhondo.
19 Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Nodabu.
20 Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m’dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.
21 Ndipo analanda zoweta zao,ngamirazao zikwi makumi asanu, ndi nkhosa zikwi mazana awiri ndi makumi asanu, ndi abulu zikwi ziwiri, ndi amuna zikwi zana limodzi.
22 Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m’malo mwao mpaka anatengedwa ndende.
Adzukulu a Manase kum’mawa
23 Ndi anthu a hafu la fuko la Manase anakhala m’dziko; anachuluka kuyambira Basani kufikira Baala-Heremoni, ndi Seniri, ndi phiri la Heremoni.
24 Ndipo akulu a nyumba za makolo ao ndi awa: Efere, ndi Isi, ndi Eliyele, ndi Aziriele, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadiyele, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.
25 Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nachita chigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m’dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.
26 Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/5-ea3c40941bf41217819a6cd5e9aa101f.mp3?version_id=1068—