Adzukulu a Yuda
1 Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala.
2 Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.
3 Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezireele, ndi Isima, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,
4 ndi Penuwele atate wa Gedori, ndi Ezere atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efurata atate wa Betelehemu.
5 Ndipo Asiriya atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.
6 Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Hefere, ndi Temeni, ndi Haahasitari. Iwo ndiwo ana a Naara.
7 Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, Izihara, ndi Etinani.
8 Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele mwana wa Harumu.
9 Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ake; ndi make anamutcha dzina lake Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.
10 Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.
11 Ndipo Kelubu mbale wa Suha anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni.
12 Ndi Esitoni, anabala Beterafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka.
13 Ndi ana a Kenazi: Otiniyele, ndi Seraya; ndi mwana wa Otiniyele: Hatati.
14 Ndipo Meonotai anabala Ofura; ndi Seraya anabala Yowabu atate wa Geharasimu; popeza iwo ndiwo amisiri.
15 Ndi ana a Kalebe mwana wa Yefune: Iru, Ela, ndi Naamu; ndi ana a Ela, ndi Kenazi.
16 Ndi ana a Yehalelele: Zifi, ndi Zifa, Tiriya, ndi Asarele.
17 Ndi ana a Ezara: Yetere, ndi Meredi, ndi Efere, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriyamu, ndi Samai, ndi Isiba atate wa Esitemowa.
18 Ndi mkazi wake Myuda anabala Yeredi atate wa Gedori, ndi Hebere atate wa Soko, ndi Yekutiyele atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi waFarao, amene Meredi anamtenga.
19 Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo atate a Keila Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka.
20 Ndi ana a Simoni; Aminoni, ndi Rina, Benihanani, ndi Tiloni. Ndi ana a Isi: Zoheti, ndi Benizoheti.
21 Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,
22 ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yowasi, ndi Sarafi wolamulira mu Mowabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.
23 Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala mu Netaimu, ndi mu Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m’ntchito yake.
Adzukulu a Simeoni
24 Ana a Simeoni: Nemuwele, ndi Yamini, Yaribu, Zera, Shaulo,
25 Salumu mwana wake, Mibisamu mwana wake, Misima mwana wake.
26 Ndi ana a Misima: Hamuele mwana wake, Zakuri mwana wake, Simei mwana wake.
27 Ndipo Simei anali nao ana aamuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana aakazi asanu ndi mmodzi; koma abale ake analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinachulukitse ngati ana a Yuda.
28 Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazara-Suwala,
29 ndi ku Biliha, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi,
30 ndi ku Betuele, ndi ku Horoma, ndi ku Zikilagi,
31 ndi ku Betemara-Kaboti, ndi ku Hazara-Susimu, ndi ku Betebiri, ndi ku Saaraimu. Iyi ndi mizinda yao, mpaka ufumu wa Davide, pamodzi ndi midzi yao.
32 Etamu, ndi Aini, Rimoni, ndi Tokeni, ndi Asani, mizinda isanu;
33 ndi midzi yao yonse pozungulira pake pa mizinda yomweyi, mpakaBaala. Apo ndi pokhala pao ndipo ali nao mawerengedwe a maina ao.
34 Ndi Mesobabu, ndi Yamuleki, ndi Yosa mwana wa Amaziya,
35 ndi Yowele, ndi Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele;
36 ndi Eliyoenai, ndi Yaakoba, ndi Yesohaya, ndi Asaya, ndi Adiyele, ndi Yesimiele, ndi Benaya,
37 ndi Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya;
38 awa otchedwa maina ndiwo akalonga m’mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao zinachuluka kwambiri.
39 Ndipo anamuka mpaka polowera ku Gedori kum’mawa kwa chigwa, kufunafuna podyetsa zoweta zao.
40 Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.
41 Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m’malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.
42 Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, ananka kuphiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uziyele; ana a Isi.
43 Nakantha otsala a Aamaleke adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/4-1db62766d48a8477f7ba150e90f9ea95.mp3?version_id=1068—