Ana a Israele, adzukulu a Yuda
1 Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni,
2 Dani, Yosefe, ndi Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere.
3 Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.
4 Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana aamuna onse a Yuda ndiwo asanu.
5 Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.
6 Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.
7 Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho.
8 Ndi mwana wa Etani: Azariya.
9 Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameele, ndi Ramu, ndi Kalebe.
10 Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;
11 ndi Nasoni anabala Salimoni, ndi Salimoni anabala Bowazi,
12 ndi Bowazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Yese,
13 ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu,
14 Netanele wachinai, Radai wachisanu,
15 Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiwiri;
16 ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu.
17 Ndi Abigaile anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yetere Mwismaele.
18 Ndi Kalebe mwana wa Hezironi anabala ana ndi Azuba mkazi wake, ndi Yerioti; ndipo ana ake ndiwo Yesere, ndi Sobabu, ndi Aridoni.
19 Namwalira Azuba, ndi Kalebe anadzitengera Efurata, amene anambalira Huri.
20 Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezalele.
21 Ndipo pambuyo pake Hezironi analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Giliyadi, amene anamtenga akhale mkazi wake, pokhala wa zaka makumi asanu ndi limodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.
22 Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo mizinda makumi awiri mphambu itatu m’dziko la Giliyadi.
23 Ndi Gesuri ndi Aramu analanda mizinda ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi midzi yake; ndiyo mizinda makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi.
24 Ndipo atafa Hezironi mu Kalebe-Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anambalira Asiriya atate wa Tekowa.
25 Ndi ana a Yerameele mwana woyamba wa Hezironi ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.
26 Ndipo Yerameele anali naye mkazi wina dzina lake ndiye Atara, ndiye make wa Onamu.
27 Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameele ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.
28 Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.
29 Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.
30 Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31 Ndi mwana wa Apaimu: Isi. Ndi mwana wa Isi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.
32 Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yetere, ndi Yonatani; namwalira Yetere wopanda ana.
33 Ndi ana a Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameele.
34 Ndipo Sesani analibe ana aamuna, koma ana aakazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata Mwejipito dzina lake ndiye Yara.
35 Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wake mwana wake wamkazi akhale mkazi wake, ndipo anambalira Atai.
36 Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,
37 ndi Zabadi anabala Efilala, ndi Efilala anabala Obedi,
38 ndi Obedi anabala Yehu, ndi Yehu anabala Azariya,
39 ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa,
40 ndi Eleasa anabala Sisimai, ndi Sisimai anabala Salumu,
41 ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.
42 Ndi ana a Kalebe mbale wa Yerameele ndiwo Mesa mwana wake woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.
43 Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema.
44 Ndi Sema anabala Rahama atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai.
45 Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betezuri.
46 Ndi Efa mkazi wamng’ono wa Kalebe anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi.
47 Ndi ana a Yadai: Regemu, ndi Yotamu, ndi Gesani, ndi Peleti, ndi Efa, ndi Saafi.
48 Maaka mkazi wamng’ono wa Kalebe anabala Sebere, ndi Tirihana.
49 Iyeyu anabalanso Saafi atate wa Madimana, Seva atate wa Makibena, ndi atate wa Gibea; ndi mwana wamkazi wa Kalebe ndiye Akisa.
50 Ana a Kalebe ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efurata, Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu.
51 Salima atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betegadere.
52 Ndipo Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu anali ndi ana: Harowe, ndi Hazi Amenuwoti.
53 Ndi mabanja a Kiriyati-Yearimu: Aitiri, ndi Aputi, ndi Asumati, ndi Amisrai; Azorati ndi Aestaoli anafuma kwa iwowa.
54 Ana a Salima: Betelehemu, ndi Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu, ndi Hazi Amanahati, ndi Azori.
55 Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/2-4575f0a87fd62aa2f3336f627c6ba32e.mp3?version_id=1068—