Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 8

Aika likasa mu Kachisi

1 Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni muYerusalemu, kukatengalikasa la chipanganocha Yehova m’mzinda wa Davide, ndiwoZiyoni.

2 Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m’mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri.

3 Ndipo akulu onse a Israele anadza, ansembe nanyamula likasa.

4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndichihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m’chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

5 Ndipo mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Israele losonkhana kwa iye linali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng’ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.

6 Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko aakerubi.

7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake.

8 Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.

9 Munalibe kanthu m’likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m’dziko la Ejipito.

10 Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m’malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova.

11 Ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

Mau a Solomoni popereka Kachisi kwa Mulungu

12 Pamenepo Solomoni anati, Yehova ananena kuti adzakhala m’mdima waukulu.

13 Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.

14 Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yake, nidalitsa msonkhano wonse wa Israele. Ndi msonkhano wonse wa Israele unaimirira.

15 Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m’kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,

16 Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m’dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.

17 Ndipo Davide atate wanga anafuna m’mtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

18 Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m’mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti m’mtima mwako unatero.

19 Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m’chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.

20 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake analankhulawo, ndipo ndauka ndine m’malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba.

21 Ndipo ndakonzera malo likasalo, m’mene muli chipangano cha Yehova, chimene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa m’dziko la Ejipito.

22 Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,

23 Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m’thambo la kumwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,

24 wakusungira mtumiki wanu Davide atate wanga chimene mudamlonjezacho; munalankhulanso m’kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.

25 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.

26 Ndipo tsopano, Mulungu wa Israele, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga.

27 Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

28 Koma mucheukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwake kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;

29 kuti maso anu atsegukire nyumba ino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.

30 Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

31 Ngati munthu akachimwira mnzake, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m’nyumba ino;

32 mverani Inu pamenepo m’mwambamo, ndipo chitani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga chilungamo chake.

33 Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m’nyumba muno;

34 pamenepo mverani Inu mu Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

35 Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;

36 pamenepo mverani Inu mu Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula padziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.

37 M’dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m’dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;

38 tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;

39 pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;

40 kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m’dziko limene Inu munapatsa makolo ao.

41 Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisraele, koma wakufumira m’dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu,

42 popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba ino;

43 mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba ino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu.

44 Akatuluka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse Inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika kumzinda uno munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

45 pamenepo mverani Inu mu Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

46 Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,

47 ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m’dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;

48 ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m’dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumzinda munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

49 pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao mu Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,

50 ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;

51 pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi cholowa chanu chimene munatulutsa mu Ejipito, m’kati mwa ng’anjo ya chitsulo;

52 kuti maso anu akatsegukire pembedzero la kapolo wanu ndi pembedzero la anthu anu Aisraele, kuwamvera m’mene monse akafuula kwa Inu.

53 Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a padziko lapansi akhale cholowa chanu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munatulutsa makolo athu mu Ejipito, Yehova Mulungu Inu.

Solomoni adalitsa Aisraele

54 Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomoni kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ake, ndi manja ake otambasulira kumwamba.

55 Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israele ndi mau okweza, nati,

56 Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisraele, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayike mau amodzi a mau ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake.

57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;

58 kuti atitembenuzire kwa Iye yekha mitima yathu iyende m’njira zake zonse, ndi kusunga malamulo ake onse ndi malemba ake ndi maweruzo ake, amene anawalamulira makolo athu.

59 Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wake, ndi mlandu wa anthu ake Aisraele, mlandu wa tsiku pa tsiku lake;

60 kuti anthu onse a padziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.

61 Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m’malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino.

62 Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israele pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova.

63 Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng’ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.

64 Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.

65 Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.

66 Tsiku lachisanu ndi chitatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israele anthu ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/8-5b38975e3a3a2c6df02695805ca42d53.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *