Nkhondo pakati pa Ahabu ndi Benihadadi
1 Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo.
2 Natumiza mithenga kumzinda kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati kwa iye,
3 Atero Benihadadi,Silivawako ndi golide wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.
4 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo.
5 Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;
6 koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m’nyumba mwako, ndi m’nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa.
7 Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza.
8 Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musavomereze.
9 Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau.
10 Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
11 Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.
12 Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m’misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamzindapo.
13 Ndipo taonani,mnenerianadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m’dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova.
14 Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe.
15 Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri.
16 Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m’misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.
17 Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, Mu Samariya mwatuluka anthu.
18 Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m’nkhondo, agwireni, amoyo.
19 Tsono anatuluka m’mzinda anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata.
20 Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo.
21 Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe aakulu.
22 Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu.
23 Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m’mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu.
24 Tsono chitani ichi, chotsani mafumu aja yense ku malo ake, muike m’malo mwao akazembe.
25 Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene.
26 Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele.
27 Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko.
28 Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m’dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.
29 Ndipo awa anakhala m’misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi.
30 Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m’mzinda, m’chipinda cha m’katimo.
31 Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m’chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.
32 Motero anavala chiguduli m’chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga.
33 Tsono anthuwo anamyang’anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m’galeta mwake.
34 Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza mizinda ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda mu Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera mu Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke.
35 Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha.
36 Ndipo ananena naye, Popeza sunamvere mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m’mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha.
37 Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha.
38 Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pake.
39 Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva,
40 Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha.
41 Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri.
42 Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m’dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m’malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m’malo mwa anthu ake.
43 Pamenepo mfumu ya Israele inanka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samariya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/20-37c338fe2b6fe8a8db8bc73014964727.mp3?version_id=1068—