Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 18

Eliya ndi Abaala ku Karimele

1 Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.

2 Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.

3 Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang’anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;

4 pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m’phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.

5 Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse.

6 Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yake yekha, ndi Obadiya njira ina yekha.

7 Ndipo Obadiya ali m’njira taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya?

8 Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

9 Iye nati, Ndachimwanji kuti mupereka kapolo wanu m’dzanja la Ahabu kundipha?

10 Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni.

11 Ndipo tsopano mukuti, Kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera.

12 Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.

13 Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m’kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m’phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?

14 Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha.

15 Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pake, zedi, ndionekadi pamaso pake lero.

16 Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya.

17 Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo?

18 Nati iye, Sindimavute Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala.

19 Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele.

20 Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israele, namemeza aneneri onse kuphiri la Karimele.

21 Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.

22 Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekhamneneriwa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.

23 Atipatse tsono ng’ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng’ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng’ombe yinayo, ndi kuiika pankhuni osasonkhapo moto.

24 Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.

25 Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Baala, Dzisankhireni ng’ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza muchuluka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto.

26 Ndipo iwo anatenga ng’ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m’mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.

27 Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka.

28 Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali chuchuchu.

29 Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.

30 Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo.

31 Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele.

32 Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m’dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mchera, ukulu wake ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.

33 Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng’ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.

34 Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu.

35 Ndipo madzi anayenda pozinga guwa la nsembe, nadzazanso mcherawo ndi madzi.

36 Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.

37 Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.

38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.

39 Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu.

40 Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.

41 Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri.

42 Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake.

43 Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri.

44 Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni.

45 Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu. Ndipo Ahabu anayenda m’galeta, namuka ku Yezireele.

46 Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m’chuuno mwake, nathamanga m’tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/18-a066bcde6a066783c5c065731f904850.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *