Mneneri Eliya ku Keriti
1 Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.
2 Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
3 Choka kuno, nutembenukire kum’mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani.
4 Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makwangwala kukudyetsa kumeneko.
5 Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani.
6 Ndipo makwangwala anamtengera mkate ndi nyama m’mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
7 Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m’dziko.
Eliya aukitsa mwana wa wamasiye ku Zarefati
8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
9 Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
10 Tsono iye ananyamuka nanka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mzinda; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang’ono m’chikho, ndimwe.
11 Ndipo m’mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m’dzanja lako.
12 Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m’mbiya, ndi mafuta pang’ono m’nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
13 Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma yamba wandiotcherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.
14 Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova padziko lapansi.
15 Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m’nyumba ake, masiku ambiri.
16 Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
17 Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yake, analeka kupuma.
18 Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
19 Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m’mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.
20 Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake?
21 Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m’chifuwa mwake.
22 Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
23 Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m’nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.
24 Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m’kamwa mwanuwo ngoona.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/17-feb934d66651e8d5cf6e90d0755b48b2.mp3?version_id=1068—