Abiya atsata zoipa za atate wake Rehobowamu
1 Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda.
2 Anakhala mfumu zaka zitatu muYerusalemu, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.
3 Nayenda iye m’zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.
4 Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali mu Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu;
5 chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.
6 Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wake.
7 Ndipo machitidwe ake ena a Abiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.
8 Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m’mzinda wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m’malo mwake.
Maweruzidwe okoma a Asa
9 Ndipo chaka cha makumi awiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda.
10 Nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi anai mphambu chimodzi, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu.
11 Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.
12 Nachotsa m’dziko anyamata aja adama, nachotsanso mafano onse anawapanga atate ake.
13 Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.
14 Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.
15 Ndipo analonga m’nyumba ya Yehova zinthu zija atate wake adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasilivandi zagolide ndi zotengera.
Nkhondo ya pakati pa Asa ndi Baasa
16 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.
17 Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.
18 Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m’nyumba ya Yehova chuma chili m’nyumba ya mfumu, nazipereka m’manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,
19 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.
20 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumizinda ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali.
21 Tsono Baasa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza.
22 Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Baasa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa.
23 Ndipo machitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yake yonse, ndi zonse anazichita, ndi mizinda anaimanga, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wake anadwala mapazi ake.
24 Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m’mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m’malo mwake.
Baasa akantha mbumba ya Yerobowamu nakhala mfumu ya Israele
25 Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.
26 Nachita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya atate wake, ndi m’tchimo lomwelo iye akachimwitsa nalo Aisraele.
27 Ndipo Baasa mwana wa Ahiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira chiwembu; ndipo Baasa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisraele onse adamangira misasa Gibetoni.
28 Inde Baasa anamupha chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m’malo mwake.
29 Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo;
30 chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.
31 Ndipo machitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?
32 Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.
33 Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai.
34 Ndipo anachimwa pamaso pa Yehova, nayenda m’njira ya Yerobowamu, ndi m’tchimo lake iye anachimwitsa nalo Israele.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/15-ceed90c0e8bb1f7e94e0a846c62ad7c8.mp3?version_id=1068—