Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 13

Mneneri adzudzula Yerobowamu

1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m’mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.

2 Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m’nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.

3 Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang’ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.

4 Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.

5 Ndiponso guwalo linang’ambika, ndi phulusa la paguwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova.

6 Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.

7 Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.

8 Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.

9 Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

10 Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele.

Mneneri wosamverayo aphedwa ndi mkango

11 Ndipo ku Betele kunakhalamneneriwokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo mu Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

12 Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo.

13 Nanena ndi ana ake, Ndimangireni mbereko pabulu. Namangira iwo mbereko pabulu, naberekekapo iye.

14 Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anachokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.

15 Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate.

16 Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;

17 pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

18 Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.

19 Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.

20 Ndipo kunachitika iwo ali chikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo,

21 nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvere mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,

22 koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.

23 Ndipo kunachitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pabulu mneneri amene anambwezayo.

24 Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m’njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.

25 Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m’njiramo, ndi mkango uli chiimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m’mzinda m’mene munakhala mneneri wokalamba uja.

26 Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.

27 Iye nanena ndi ana ake, nati, Ndimangireni mbereko pabulu. Namangira mbereko.

28 Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m’njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.

29 Ndipo mneneri ananyamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pabulu, nabwera nao, nalowa m’mzinda mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.

30 Ndipo mtembo wake anauika m’manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!

31 Ndipo kunachitika, atamuika iye, ananena ndi ana ake, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m’manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ake.

32 Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m’mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.

33 Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere panjira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje.

34 Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga padziko lapansi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/13-c686484e846f8b4e0efabb57a67ede4a.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *