Rehobowamu samvera uphungu wa akulu
1 Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.
2 Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali mu Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito.
3 Ndipo anatuma kukamuitana. Ndipo Yerobowamu ndi msonkhano wonse wa Israele anadza, nalankhulana ndi Rehobowamu, nati,
4 Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.
5 Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka.
6 Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?
7 Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala chikhalire atumiki anu.
8 Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake,
9 nati kwa iwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenza ife?
10 Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m’chuuno mwa atate wanga.
11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
12 Ndipo Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu.
13 Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,
14 nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
15 Potero mfumu siinamvere anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.
16 Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m’mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang’aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.
17 Koma ana aja a Israele akukhala m’mizinda ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao.
18 Pamenepo mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehobowamu anafulumira kulowa m’galeta wake kuthawira kuYerusalemu.
19 Motero Aisraele anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.
20 Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda.
21 Ndipo Rehobowamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi fuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israele, kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni.
22 Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semayamneneriwa Mulungu, nati,
23 Lankhula kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,
24 Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.
Kupembedza mafano kwa Yerobowamu
25 Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m’mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.
26 Ndipo Yerobowamu ananena m’mtima mwake, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide.
27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m’nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda.
28 Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang’ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m’dziko la Ejipito.
29 Ndipo anaimika mmodzi ku Betele, naimika wina ku Dani.
30 Koma chinthu ichi chinasanduka tchimo, ndipo anthu ananka ku mmodziyo wa ku Dani.
31 Iye namanga nyumba za m’misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.
32 Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe paguwa la nsembe; anatero mu Betele, nawaphera nsembe anaang’ombe aja anawapanga, naika mu Betele ansembe a misanje imene anaimanga.
33 Ndipo anapereka nsembe paguwa la nsembe analimanga mu Betele, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chitatu, m’mwezi umene anaulingirira m’mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israele madyerero, napereka nsembe paguwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/12-c0e79f61082c4b47edb3093168dfd90e.mp3?version_id=1068—