Mau Oyamba
Kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto
inalembedwa pofuna kukonza mavuto okhudzana ndi moyo wa Chikhristu komanso chikhulupiriro amene anabuka mu mpingo umene Paulo anakhazikitsa ku Korinto. Mu nthawi imeneyo, unali mzinda waukulu Wachigriki wa malonda, ndipo unali likulu la dera la Akaya. Mzindawu umadziwika ndi malonda osiyanasiyana, miyambo yake yosiririka, za dama ndi zipembedzo zosiyanasiyana.
Nkhawa yaikulu ya mtumwi inali mavuto amene analipo, monga kugawikana ndi chigololo komanso mafunso okhudzana ndi kugonana ndi banja, chikumbumtima, dongosolo la mu mpingo, mphatso za Mzimu Woyera ndi kuuka kwa akufa. Paulo akugwiritsa ntchito Uthenga Wabwino pofuna kufotokozera zonsezi bwino lomwe.
Mu mutu 13, pamene akukamba za chikondi ngati mphatso ya mtengo wapatali ya Mulungu kwa anthu ake. Imeneyi ndi ndime yodziwika bwino mu bukuli.
Za mkatimu
Mau oyamba 1.1-9
Kugawana mu mpingo 1.10—4.21
Za moyo wabanja ndikugonana koyenera 5.1—7.40
Akhristu ndi akunja 8.1—11.1
Moyo ndi chipembedzo cha mu mpingo 11.2—14.40
Kuukanso kwa Yesu ndi kwa okhulupirira 15.1-58
Chopereka cha Akhristu a ku Yudeya 16.1-4
Malonje ndi mau omaliza 16.5-24