Awadzudzula pa milandu ya pakati pa abale
1 Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?
2 Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa?
3 Kodi simudziwa kuti tidzaweruzaangelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?
4 Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe muMpingo?
5 Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,
6 koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?
7 Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?
8 Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.
9 Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,
10 kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
11 Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye YesuKhristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.
Matupi athu ali ziwalo za Khristu
12 Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.
13 Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;
14 koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.
15 Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai.
16 Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.
17 Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.
18 Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.
19 Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.
20 Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/6-b5158dd682c61c8a882f6284dbf8cfc3.mp3?version_id=1068—