Za kuuka kwa akufa
1 Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo,
2 umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.
3 Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kutiKhristuanafera zoipa zathu, monga mwa malembo;
4 ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo;
5 ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;
6 pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;
7 pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwaatumwionse;
8 ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.
9 Pakuti ine ndili wamng’ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalondaMpingowa Mulungu.
10 Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.
11 Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira.
12 Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa?
13 Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe;
14 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.
15 Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitse, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.
16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwe;
17 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m’machimo anu.
18 Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika.
19 Ngati tiyembekezera Khristu m’moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.
20 Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.
21 Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu.
22 Pakuti monga mwaAdamuonse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.
23 Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.
24 Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe.
25 Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.
26 Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.
27 Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye.
28 Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
29 Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?
30 Nanga ifenso tili m’moopsa bwanji nthawi zonse?
31 Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwaKhristuYesu, Ambuye wathu.
32 Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.
33 Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.
34 Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
35 Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani?
36 Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa;
37 ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina;
38 koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake.
39 Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba.
40 Palinso matupi am’mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam’mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso.
41 Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi mu ulemerero.
42 Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chivundi, liukitsidwa m’chisavundi;
43 lifesedwa m’mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m’chifooko, liukitsidwa mumphamvu;
44 lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.
45 Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.
46 Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.
47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.
48 Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba.
49 Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo.
50 Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.
51 Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika,
52 m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.
53 Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa.
54 Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m’chigonjetso.
55 Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti?
56 Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo:
57 koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
58 Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/15-2f7b137e8c952e88d37426bd21f54b15.mp3?version_id=1068—