Mphatso ya kunenera iposa ya malilime
1 Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere.
2 Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.
3 Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.
4 Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangiriraMpingo.
5 Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.
6 Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m’vumbulutso, kapena m’chidziwitso, kapena m’chinenero, kapena m’chiphunzitso?
7 Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa?
8 Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?
9 Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.
10 Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau padziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau.
11 Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.
12 Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.
13 Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.
14 Pakuti ngati ndipemphera m’lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu.
15 Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.
16 Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzatiAmenbwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?
17 Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwe.
18 Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse;
19 koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m’lilime.
20 Abale, musakhale ana m’chidziwitso, koma m’choipa khalani makanda, koma m’chidziwitso akulu misinkhu.
21 Kwalembedwa m’chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.
22 Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.
23 Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?
24 Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse;
25 zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
Chipembedzo chichitike molongosoka
26 Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.
27 Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire.
28 Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
29 Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire.
30 Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo.
31 Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe;
32 ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri;
33 pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
34 Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.
35 Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo.
36 Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha?
37 Ngati wina ayesa kuti alimneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
38 Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.
39 Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.
40 Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/14-73ce4af24a4d9a4a6d78295b4fe5a292.mp3?version_id=1068—