Kuposa kwa Chikondi
1 Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi aangelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
2 Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.
3 Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.
4 Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
5 sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
6 sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi;
7 chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
8 Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.
9 Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera.
10 Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.
11 Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.
12 Pakuti tsopano tipenya m’kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
13 Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CO/13-59be74f2e331cc2e9e24b4a393cdee84.mp3?version_id=1068—